-
Yoswa 8:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano mfumu ya Ai itangoona zimenezo, amuna a mumzindawo anakonzekera msangamsanga. M’mawa mwake analawirira kuti akamenyane ndi Aisiraeli. Mfumuyo limodzi ndi anthu ake onse, ananyamuka pa nthawi imene anapangana, ndipo analowera kuchigwa cha m’chipululu. Koma mfumuyo sinadziwe kuti asilikali ena anali atabisala kumbuyo kwa mzindawo.+
-