-
Genesis 37:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Ndiyeno anakhala pansi kuti adye chakudya.+ Koma pamene anakweza maso, anaona gulu la apaulendo la Aisimaeli.+ Anali kuchokera ku Giliyadi, ndipo ngamila zawo zinali zitanyamula mafuta onunkhira a labidanamu ndi a basamu, komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Apaulendowo anali kupita ku Iguputo.
-
-
Genesis 43:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Chabwino, ngati ndi choncho,+ chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali za dziko lino m’matumba anu, mukam’patse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pang’ono, uchi+ pang’ono, mafuta onunkhira a labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho, ndi zipatso za amondi.+
-