Yeremiya 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu. Yeremiya 23:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Dzikoli ladzaza+ ndi anthu achigololo+ ndipo chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+ ndipo malo a m’chipululu odyetsera ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo. Hoseya 7:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Anthu onsewo ndi achigololo.+ Ali ngati ng’anjo yamoto imene wophika mkate waiyatsa. Ng’anjoyo yatentha kwambiri moti iye sakufunikira kuisonkhezera pamene akukanda ufa ndi kudikira kuti ufufume.
7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi? Ana ako aamuna andisiya ndipo amalumbira+ pa zinthu zina osati Mulungu.+ Ndinali kuwapatsa zofuna zawo+ koma anapitiriza kuchita chigololo+ ndipo anali kupita kunyumba ya hule m’magulumagulu.
10 Dzikoli ladzaza+ ndi anthu achigololo+ ndipo chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+ ndipo malo a m’chipululu odyetsera ziweto auma.+ Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo mopanda chilungamo.
4 Anthu onsewo ndi achigololo.+ Ali ngati ng’anjo yamoto imene wophika mkate waiyatsa. Ng’anjoyo yatentha kwambiri moti iye sakufunikira kuisonkhezera pamene akukanda ufa ndi kudikira kuti ufufume.