16 “Choncho Yehova, Mulungu wa makamu, Yehova wanena kuti, ‘Padzamveka kulira m’mabwalo onse a mizinda+ yanu ndipo m’misewu yanu yonse anthu azidzanena kuti: “Aa! Aa!” Pamenepo adzaitana mlimi kuti alire+ ndiponso anthu odziwa kulira maliro kuti alire mokweza.’+