4 Pakuti inu mwakhala malo achitetezo kwa munthu wonyozeka ndiponso malo achitetezo kwa munthu wosauka m’masautso ake.+ Mwakhala malo ousapo mvula yamkuntho ndi mthunzi+ wobisalirapo kutentha kwa dzuwa. Mwakhala wotero pamene anthu ankhanza akuwomba anzawo ngati mvula yamkuntho yowomba khoma.