8 Ndipo Yehova anapereka adaniwo m’manja mwa Aisiraeli.+ Chotero anayamba kuwapha ndi kuwathamangitsa mpaka kukafika kumzinda wa anthu ambiri wa Sidoni,+ ku Misirepotu-maimu+ ndi kuchigwa cha Mizipe+ kum’mawa. Anapitiriza kuwapha moti panalibe amene anapulumuka.+