12 Anthu achilendo, olamulira ankhanza a mitundu ina, adzadula mtengowo ndipo anthu adzausiya m’mapiri. Masamba ake adzagwera m’zigwa zonse ndipo nthambi zake zidzathyoka ndi kugwera m’mitsinje ya padziko lapansi.+ Mitundu yonse ya anthu a padziko lapansi idzachoka mumthunzi wake n’kuusiya.+