24 “‘Kumandako n’kumene kuli Elamu+ ndi khamu lake lonse. Khamu lakelo linaikidwa mozungulira manda ake. Onsewo anaphedwa ndi lupanga. Iwo anatsikira kunthaka ali osadulidwa. Amenewa anachititsa mantha anthu m’dziko la anthu amoyo, ndipo adzanyozeka limodzi ndi onse otsikira kudzenje.+