9 Ana a Isiraeli anayamba kuchita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo,+ ndipo anapitiriza kumanga malo okwezeka+ m’mizinda yawo yonse, kuyambira kunsanja+ ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
14 Komanso, anthu ndi atsogoleri onse a ansembe+ anachita zosakhulupirika zochuluka kwambiri mofanana ndi zonyansa zonse+ za anthu a mitundu ina. Choncho iwo anaipitsa nyumba ya Yehova imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.+