23 Ana a Amoni ndi ana a Mowabu anaukira anthu okhala kudera lamapiri la Seiri+ ndipo anawapha ndi kuwamaliza. Atatha kupha anthu a ku Seiri, iwo anaphana okhaokha.+
22 Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+