41 Ndiyeno munthu uja ananditengera m’kachisi. Mmenemo anayamba kuyeza zipilala zam’mbali. Chipilala china chinali mbali ya kumanzere ndipo china mbali ya kudzanja lamanja. Chipilala chilichonse chinali mikono 6 m’lifupi. Umenewu ndiwo unali muyezo wa chipilala chilichonse m’lifupi mwake.