2 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Chipata ichi chizikhalabe chotseka. Sichidzatsegulidwa, ndipo munthu wamba sadzalowa kudzera pachipata chimenechi chifukwa chakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli,+ walowa kudzera pachipata chimenechi. Choncho chidzapitirizabe kukhala chotseka.