20 ‘Utengeko magazi akewo n’kuwapaka panyanga zinayi za guwa lansembe ndi m’makona anayi a chigawo chachitatu cha guwalo. Magaziwo uwapakenso pakakhoma konse kozungulira chigawo chachitatucho. Uchite zimenezi kuti uyeretse guwa lansembelo ku machimo+ ndipo uliperekere nsembe yophimba machimo.+