7 Solomo anapatula+ malo a pakati pa bwalo la nyumba ya Yehova, chifukwa pamenepo anaperekerapo nsembe zopsereza,+ ndi mafuta a nsembe zachiyanjano. Anatero popeza guwa lansembe lamkuwa+ limene iye anamanga linachepa, ndipo sipakanakwana nsembe yopsereza, nsembe yambewu,+ ndi mafuta oundana.+