3 Iweyo sudzazemba kuti asakugwire chifukwa adzakugwira ndithu ndi kukupereka m’manja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo+ maso ndi maso, ndipo idzalankhula nawe ndi kupita nawe ku Babulo.’
11 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga ndi maunyolo amkuwa n’kupita naye ku Babulo.+ Kumeneko anamuika m’ndende mpaka tsiku la imfa yake.