43 Pa nthawiyo, adzakhala atasiya dziko lawo, ndipo dzikolo lidzakhala likubweza masabata ake+ pamene lidzakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo adzakhala akulipira chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa chakuti anakana zigamulo zanga+ ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+