Genesis 41:45 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 45 Farao atatero, anapatsa Yosefe dzina lakuti, Zafenati-panea.* Anam’patsanso mkazi dzina lake Asenati.+ Mtsikanayu anali mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.+ Pamenepo Yosefe anayamba kuyendera dziko la Iguputo.+ 2 Mafumu 23:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Kuwonjezera apo, Farao Neko anaika Eliyakimu+ mwana wa Yosiya kukhala mfumu m’malo mwa Yosiya bambo ake, n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Atatero anatenga Yehoahazi n’kupita naye ku Iguputo, kumene anakafa pamapeto pake.+ 2 Mafumu 24:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Komanso mfumu ya Babulo+ inatenga Mataniya, bambo ake aang’ono+ a Yehoyakini, n’kuwaika kukhala mfumu m’malo mwake. Kenako inam’sintha dzina Mataniya kuti akhale Zedekiya.+
45 Farao atatero, anapatsa Yosefe dzina lakuti, Zafenati-panea.* Anam’patsanso mkazi dzina lake Asenati.+ Mtsikanayu anali mwana wa Potifera, yemwe anali wansembe wa mzinda wa Oni.+ Pamenepo Yosefe anayamba kuyendera dziko la Iguputo.+
34 Kuwonjezera apo, Farao Neko anaika Eliyakimu+ mwana wa Yosiya kukhala mfumu m’malo mwa Yosiya bambo ake, n’kumusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Atatero anatenga Yehoahazi n’kupita naye ku Iguputo, kumene anakafa pamapeto pake.+
17 Komanso mfumu ya Babulo+ inatenga Mataniya, bambo ake aang’ono+ a Yehoyakini, n’kuwaika kukhala mfumu m’malo mwake. Kenako inam’sintha dzina Mataniya kuti akhale Zedekiya.+