25 Chifukwa cha kuzindikira kwake idzathadi kugwiritsa ntchito chinyengo.+ Idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake,+ ndipo idzawononga anthu ambiri pa nthawi imene zinthu zikuiyendera bwino.+ Mfumuyo idzalimbana ndi Kalonga wa akalonga,+ ndipo idzathyoledwa koma osati ndi dzanja la munthu.+