-
2 Mafumu 17:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Pamalo okwezeka onsewo, iwo anapitiriza kufukizapo nsembe yautsi, mofanana ndi mitundu+ imene Yehova anaithamangitsa m’dzikolo chifukwa cha Aisiraeliwo. Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa zokwiyitsa+ Yehova.
-
Ezekieli 6:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+
-
-
-