6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
13 Yehova anapitiriza kunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ana a Isiraeli azidzadya chakudya chodetsedwa+ pakati pa mitundu yosiyanasiyana imene ndidzawathamangitsireko.”+