10 Pamapeto pa zaka zitatu, Asuriwo analanda mzindawo.+ Anaulanda m’chaka cha 6 cha Hezekiya, kutanthauza chaka cha 9 cha Hoshiya mfumu ya Isiraeli. Chotero Samariya analandidwa.+
16 “Samariya adzaimbidwa mlandu+ chifukwa iye akupandukira Mulungu wake.+ Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+ Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa+ ndipo akazi awo amene ali ndi pakati adzatumbulidwa.”+