Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 15:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ndipo muzikapereka vinyo monga nsembe yachakumwa.+ Azikakhala wokwanira gawo limodzi mwa magawo anayi a muyezo wa hini. Vinyoyo muzikam’pereka limodzi ndi nsembe yopsereza, kapena ndi nsembe ya mwana wa nkhosa wamphongo.

  • Numeri 28:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Panyama iliyonse yoperekedwa nsembe muziperekanso nsembe yachakumwa. Ng’ombe yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana hafu+ ya muyezo wa hini. Nkhosa yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu+ a muyezo wa hini. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo muzim’pereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo anayi+ a muyezo wa hini. Zinthu zimenezi muzizipereka monga nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, yoperekedwa mwezi uliwonse pa miyezi yonse ya pa chaka.+

  • Yoweli 1:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 “Dzimangirireni m’chiuno ndipo dzigugudeni pachifuwa,+ inu ansembe. Lirani mofuula, inu atumiki a paguwa lansembe.+ Lowani, valani ziguduli usiku wonse inu atumiki a Mulungu wanga, pakuti nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa zachotsedwa m’nyumba ya Mulungu wanu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena