10 “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa umene ukuwonongeka.+ Iye akupitiriza kubereka zipatso+ ndipo wachulukitsa maguwa ansembe mogwirizana ndi kuchuluka kwa zipatso zake.+ Pamene dzikolo likutukuka kwambiri m’pamenenso Aisiraeli akumanga zipilala zopatulika zokongola kwambiri.+