Yesaya 10:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Kodi anthu inu mudzatani pa tsiku limene adzatembenukire kwa inu+ ndi kukubweretserani chiwonongeko chochokera kutali?+ Mudzathawira kwa ndani kuti akuthandizeni+ ndipo ulemerero wanu mudzausiya kuti?+ Ezekieli 12:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Chotero uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndithu Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’+ Koma uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo zonse zotchulidwa m’masomphenya zichitikadi.’ Hoseya 9:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 “Masiku oti uyenderedwe adzafika,+ masiku oti ulipire adzakwana+ ndipo anthu a Isiraeli adzadziwa zimenezi.+ Mneneri adzapusa+ ndipo munthu wolankhula mawu ouziridwa adzalusa, chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako+ ndiponso chifukwa cha kuchuluka kwa chidani.”
3 Kodi anthu inu mudzatani pa tsiku limene adzatembenukire kwa inu+ ndi kukubweretserani chiwonongeko chochokera kutali?+ Mudzathawira kwa ndani kuti akuthandizeni+ ndipo ulemerero wanu mudzausiya kuti?+
23 Chotero uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndithu Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’+ Koma uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo zonse zotchulidwa m’masomphenya zichitikadi.’
7 “Masiku oti uyenderedwe adzafika,+ masiku oti ulipire adzakwana+ ndipo anthu a Isiraeli adzadziwa zimenezi.+ Mneneri adzapusa+ ndipo munthu wolankhula mawu ouziridwa adzalusa, chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako+ ndiponso chifukwa cha kuchuluka kwa chidani.”