-
Deuteronomo 16:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 “Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe.+ Azikaonekera pa chikondwerero cha mkate wopanda chofufumitsa,+ chikondwerero cha masabata+ ndi pa chikondwerero cha misasa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa Yehova chimanjamanja.+
-
-
Nehemiya 10:33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Akazigwiritsire ntchito pokonza mkate wosanjikiza,+ nsembe yachikhalire yambewu,+ nsembe yachikhalire yopsereza ya pa tsiku la sabata+ ndi tsiku lokhala mwezi.+ Akazigwiritsirenso ntchito pokonza madyerero a pa nthawi yoikidwiratu,+ zinthu zopatulika+ ndi nsembe yamachimo+ yophimbira machimo a Isiraeli komanso pa ntchito zonse za panyumba ya Mulungu wathu.+
-