Yesaya 14:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Ngakhale mitengo ya mlombwa+ yakondwa poona zimene zakuchitikira. Nayonso mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni yakondwa, ndipo yonseyi yanena kuti, ‘Kuyambira pamene unagona pansi, palibenso munthu wodula mitengo+ amene wabwera kudzatidula.’ Zekariya 11:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Lira mofuula, iwe mtengo wofanana ndi mkungudza, chifukwa chakuti mtengo wa mkungudza wagwa, ndiponso mitengo ikuluikulu yawonongedwa.+ Lirani mofuula, inu mitengo ikuluikulu ya ku Basana, chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.+
8 Ngakhale mitengo ya mlombwa+ yakondwa poona zimene zakuchitikira. Nayonso mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni yakondwa, ndipo yonseyi yanena kuti, ‘Kuyambira pamene unagona pansi, palibenso munthu wodula mitengo+ amene wabwera kudzatidula.’
2 Lira mofuula, iwe mtengo wofanana ndi mkungudza, chifukwa chakuti mtengo wa mkungudza wagwa, ndiponso mitengo ikuluikulu yawonongedwa.+ Lirani mofuula, inu mitengo ikuluikulu ya ku Basana, chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.+