Yesaya 34:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+ Yeremiya 4:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Ndinaona mapiri ndipo anali kugwedezeka. Zitunda zonse zinali kunjenjemera.+ Yoweli 3:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+ Aheberi 12:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.”+
4 Makamu onse akumwamba adzawola.+ Kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu wolembapo.+ Makamu onse akumwambawo adzafota ngati mmene masamba amafotera pamtengo wa mpesa n’kuthothoka, ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.+
16 Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+
26 Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokhali.”+