Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 5:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 N’chifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake ndipo adzatambasula dzanja lake n’kuwapha.+ Mapiri adzanjenjemera+ ndipo mitembo yawo idzakhala ngati zinyalala m’misewu.+

      Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.

  • Ezekieli 38:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Chifukwa cha ine, nsomba zam’nyanja, zolengedwa zouluka zam’mlengalenga, zilombo zakutchire, zokwawa zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse amene ali padziko lapansi, adzanjenjemera.+ Mapiri adzagwetsedwa,+ misewu yotsetsereka idzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi.’

  • Nahumu 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mapiri agwedezeka chifukwa cha iye ndipo zitunda zasungunuka.+

      Dziko lapansi, nthaka ndi zinthu zonse zokhala m’dzikomo zidzanjenjemera.+

  • Habakuku 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Iye anaima chilili kuti agwedeze dziko lapansi.+ Anayang’ana mitundu ya anthu ndipo mitunduyo inadumpha.+

      Mapiri amuyaya anaphwanyidwa.+ Zitunda zimene zidzakhalapo mpaka kalekale* zinawerama.+ Zimenezi ndi njira zake zakalekale.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena