7 Ndidzachotsa zinthu zake zamagazi m’kamwa mwake ndipo ndidzachotsa chakudya chake chonyansa pakati pa mano ake.+ Aliyense amene adzatsale adzakhala wa Mulungu wathu. Wotsalayo adzakhala ngati mfumu+ mu Yuda,+ ndipo Ekironi adzakhala ngati Myebusi.+