2 Mbiri 6:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Mumve mapemphero ochonderera a mtumiki+ wanu ndi a anthu anu Aisiraeli, pamene akupemphera atayang’ana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+ Salimo 28:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+ Yeremiya 31:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Adzabwera akulira,+ ndipo ndidzayankha kuchonderera kwawo kuti ndiwakomere mtima. Ndidzawayendetsa kupita kuzigwa za madzi.+ Ndidzawayendetsa m’njira zabwino mmene sadzapunthwa. Pakuti ine ndakhala Tate wa Isiraeli,+ ndipo Efuraimu ndi mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa.”+
21 Mumve mapemphero ochonderera a mtumiki+ wanu ndi a anthu anu Aisiraeli, pamene akupemphera atayang’ana malo ano.+ Inuyo mumve muli kumalo anu okhala, kumwamba,+ ndipo mumve n’kukhululuka.+
2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+
9 Adzabwera akulira,+ ndipo ndidzayankha kuchonderera kwawo kuti ndiwakomere mtima. Ndidzawayendetsa kupita kuzigwa za madzi.+ Ndidzawayendetsa m’njira zabwino mmene sadzapunthwa. Pakuti ine ndakhala Tate wa Isiraeli,+ ndipo Efuraimu ndi mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa.”+