Masalimo
Salimo la Davide.
Inu Thanthwe langa, musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana,+
Kuti musakhale chete pamaso panga,+
Kutinso ine ndisafanane ndi amene akutsikira kudzenje la manda.+
2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,
Pamene ndikukweza manja anga,+ nditayang’ana kumene kuli chipinda chamkati cha m’malo anu opatulika.+
3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa komanso anthu amene amachita zopweteka anzawo,+
Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo+ koma m’mitima yawo muli zinthu zoipa.+
4 Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+
Mogwirizana ndi kuipa kwa zochita zawo.+
Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+
Abwezereni zochita zawo.+
5 Pakuti iwo salabadira zochita za Yehova,+
Kapena ntchito za manja ake.+
Mulungu sadzawamanga koma adzawapasula.
6 Adalitsike Yehova, chifukwa wamva kuchonderera kwanga.+
7 Yehova ndiye mphamvu yanga+ ndi chishango changa.+
Mtima wanga umam’khulupirira.+
Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukukondwera.+
Ndidzamutamanda mwa kumuimbira nyimbo yanga.+