Masalimo
Salimo la Davide.
27 Yehova ndiye kuwala+ kwanga ndi chipulumutso changa.+
Ndingaopenso ndani?+
Yehova ndiye malo a chitetezo cha moyo wanga.+
Ndingachitenso mantha ndi ndani?+
2 Anthu ochita zoipa atandiyandikira kuti adye mnofu wanga,+
Popeza kuti iwo ndi ondiukira komanso adani anga,+
Anapunthwa ndi kugwa.+
3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,+
Mtima wanga sudzachita mantha.+
Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,+
Pameneponso ndidzadalira Mulungu.+
4 Chinthu chimodzi chimene ndapempha kwa Yehova,+
Chimenecho ndi chimene ndimachikhumba,+
N’chakuti, ndikhale m’nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+
Kuti ndione ubwino wa Yehova,+
Komanso kuti ndiyang’ane kachisi wake moyamikira.+
5 Pakuti pa tsiku la tsoka, iye adzandibisa m’malo ake otetezeka.+
Adzandibisa m’malo obisika m’hema wake.+
Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+
6 Pamenepo mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani onse ondizungulira.+
Ndipo ndidzapereka nsembe za kufuula mokondwera pahema wake.+
Ndidzamuimbira nyimbo, ndithu ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.+
8 Mtima wanga wanena lamulo lanu lakuti: “Ndifunefuneni anthu inu.”+
Ndidzakufunafunani, inu Yehova.+
Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.+
Inu mukhale mthandizi wanga.+
Musanditaye ndi kundisiya, inu Mulungu wa chipulumutso changa.+
11 Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende m’njira yanu.+
Nditsogolereni m’njira yowongoka kuti nditetezeke kwa adani anga.
12 Musandipereke kwa adani anga.+
Pakuti mboni zonama zandiukira,+
Chimodzimodzinso munthu wachiwawa.+
13 Ngati ndikanakhala wopanda chikhulupiriro poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya chiyembekezo.+