Ekisodo 28:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 “Upangenso kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti, ‘Chiyero n’cha Yehova.’+ Ekisodo 39:30 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 30 Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Chiyero n’cha Yehova.”+ Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo. Yesaya 35:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo.
36 “Upangenso kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti, ‘Chiyero n’cha Yehova.’+
30 Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kaphanthiphanthi kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Chiyero n’cha Yehova.”+ Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.
8 Kumeneko kudzakhala msewu waukulu+ ndipo udzatchedwa Msewu wa Chiyero.+ Munthu wodetsedwa sadzayendamo.+ Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera. Palibe anthu opusa amene azidzayendayendamo.