Hagai 2:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+ Maliko 13:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 “Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomezi+ m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.+ Chivumbulutso 6:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.+
22 Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+
8 “Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomezi+ m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.+
4 Pamenepo, hatchi ina inatulukira. Imeneyi inali yofiira ngati moto. Wokwerapo wake analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi, kuti anthu aphane. Iye anapatsidwanso lupanga lalikulu.+