Salimo 55:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Umutulire Yehova nkhawa zako,+Ndipo iye adzakuchirikiza.+Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.+ 1 Timoteyo 6:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.+ Aheberi 13:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+ 1 Petulo 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Chitani zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ pakuti amakuderani nkhawa.+
5 Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama,+ koma mukhale okhutira+ ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Pakuti Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.”+