24 Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya+ monse. Anthu anamubweretsera onse amene sanali kumva bwino m’thupi,+ amene anali kuvutika ndi matenda komanso zowawa zamitundumitundu, ogwidwa ndi ziwanda, akhunyu,+ ndi anthu akufa ziwalo, ndipo iye anawachiritsa.