Mateyu 14:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita, anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.+ Ngakhale kuti kunali kutada, iye anakhalabe kumeneko yekhayekha. Maliko 14:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikukapemphera.”+ Aheberi 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+
23 Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita, anakwera m’phiri yekhayekha kukapemphera.+ Ngakhale kuti kunali kutada, iye anakhalabe kumeneko yekhayekha.
32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikukapemphera.”+
7 Pamene anali munthu, Khristu anapereka mapemphero opembedzera ndi opempha,+ kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula+ komanso akugwetsa misozi, ndipo anamumvera chifukwa chakuti anali kuopa Mulungu.+