Mateyu 26:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Kenako Yesu anafika nawo pamalo+ otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.”+ Luka 22:39 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 39 Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi monga anali kuchitira nthawi zonse. Ophunzira nawonso anamutsatira.+ Yohane 18:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Atanena zimenezi, Yesu anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwoloka khwawa la Kidironi,+ kupita kumene kunali munda. Ndipo iye ndi ophunzira akewo analowa m’mundamo.+
36 Kenako Yesu anafika nawo pamalo+ otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.”+
39 Atachoka kumeneko anapita kuphiri la Maolivi monga anali kuchitira nthawi zonse. Ophunzira nawonso anamutsatira.+
18 Atanena zimenezi, Yesu anatuluka pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwoloka khwawa la Kidironi,+ kupita kumene kunali munda. Ndipo iye ndi ophunzira akewo analowa m’mundamo.+