19 Mulungu akadzaimirira kuti dziko lapansi linjenjemere, anthu adzalowa m’mapanga a m’matanthwe ndi m’mayenje a m’nthaka chifukwa cha kuopsa kwa Yehova,+ ndiponso chifukwa cha ulemerero ndi ukulu wake.+
8 Malo okwezeka a ku Beti-aveni,+ omwe ndi tchimo la Isiraeli,+ adzawonongedwa. Minga ndi zitsamba zobaya*+ zidzamera pamaguwa awo ansembe.+ Anthu adzauza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+