29 Dziwani kuti Yehova wakupatsani sabata.+ N’chifukwa chake akukupatsani mkate wa masiku awiri pa tsiku la 6. Pa tsiku la 7 aliyense azikhala pamalo ake.+ Munthu asachoke pamalo ake.”
15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la sabata adzaphedwa ndithu.