19 Pa tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlunguwo,+ ophunzirawo anasonkhana pamodzi madzulo. Iwo anali atakhoma zitseko m’nyumba imene analimo chifukwa choopa+ Ayuda, ndipo Yesu anafika+ n’kuimirira pakati pawo ndi kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+