Ekisodo 22:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+ Levitiko 25:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 Musam’kongoze ndalama kuti adzabweze chiwongoladzanja,+ ndipo musakongoze chakudya chanu mwa kuchititsa katapira. Deuteronomo 23:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Mlendo+ ungamulipiritse chiwongoladzanja, koma m’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa zochita zako zonse m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+ Salimo 37:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Tsiku lililonse amakomera mtima ena ndi kuwakongoza zinthu,+Ndipo ana ake adzalandira madalitso.+
25 “Ukabwereketsa ndalama kwa anthu anga, kwa munthu wovutika amene ali pafupi ndi iwe,+ usakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira* kwa iye. Usafunepo chiwongoladzanja.+
37 Musam’kongoze ndalama kuti adzabweze chiwongoladzanja,+ ndipo musakongoze chakudya chanu mwa kuchititsa katapira.
20 Mlendo+ ungamulipiritse chiwongoladzanja, koma m’bale wako usamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wako akudalitse pa zochita zako zonse m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako.+