Ekisodo 32:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.+ Iye anati: “N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu+ uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu? Yoweli 2:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 “Ansembe ndi atumiki a Yehova alire m’khonde mwa guwa lansembe+ ndipo anene kuti, ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu ndipo musachititse manyazi cholowa chanu+ kuti mitundu ya anthu iwalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+
11 Pamenepo Mose anakhazika pansi mtima wa Yehova Mulungu wake.+ Iye anati: “N’chifukwa chiyani, inu Yehova, mukufuna kuti mkwiyo wanu+ uyakire anthu anu, amene munawatulutsa m’dziko la Iguputo mwa mphamvu zazikulu ndiponso ndi dzanja lamphamvu?
17 “Ansembe ndi atumiki a Yehova alire m’khonde mwa guwa lansembe+ ndipo anene kuti, ‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu ndipo musachititse manyazi cholowa chanu+ kuti mitundu ya anthu iwalamulire. Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+