15Mwamsanga m’bandakucha, ansembe aakulu, akulu ndi alembi, kutanthauza Khoti lonse Lalikulu la Ayuda,* anasonkhana pamodzi ndi kugwirizana chimodzi.+ Kenako anamanga Yesu ndi kukam’pereka kwa Pilato.+
13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza+ Mtumiki+ wake Yesu, amene inu munamupereka+ ndi kumukana pamaso pa Pilato, Pilatoyo akufuna kumumasula.+