7 “Ndidzakwaniritsa pangano langa la pakati pa ine ndi iwe,+ ndi mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe ku mibadwomibadwo. Lidzakhala pangano mpaka kalekale,+ kusonyeza kuti ndine Mulungu wako ndi wa mbewu yako yobwera pambuyo pa iwe.+
16 Koma tsopano akufunitsitsa malo abwino koposa, amene ndi malo akumwamba.+ Pa chifukwa chimenechi, Mulungu sachita nawo manyazi kuti azimuitana monga Mulungu wawo,+ pakuti iye wawakonzera mzinda.+