3 Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mu mpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira+ mu mkwiyo wanga kuti, ‘Sadzalowa+ mu mpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti ntchito zake zinali zitatha+ kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa.+