25 Tsopano Mulungu+ angakulimbitseni mwa uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso mwa uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthenga wabwino umenewu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kuyambira nthawi zakale.