17 Mu uthenga wabwinowu, chilungamo+ cha Mulungu chimaululidwa chifukwa cha chikhulupiriro cha munthu.+ Zikatero, chikhulupiriro cha munthuyo chimalimbanso monga mmene Malemba amanenera kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.”+