5 Patapita kanthawi, panafika mwana wamkazi wa Farao kudzasamba mumtsinje wa Nailo. Ndipo atsikana omutumikira anali kuyenda m’mphepete mwa mtsinjewo. Kenako iye anaona kabokosi kaja kali pakati pa mabango. Nthawi yomweyo anatuma kapolo wake wamkazi kuti akakatenge.+