13Tsopano mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneri+ ndi aphunzitsi. Iwo anali Baranaba, Sumeoni wotchedwa Nigeri, Lukiyo+ wa ku Kurene, Manayeni amene anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo, ndi Saulo.
1Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu,+ amene muli alendo osakhalitsa,+ amene mwamwazikana+ ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia, ndi ku Bituniya.